Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 10:10 - Buku Lopatulika

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Dziwani tsono, kuti sikadzagwa pansi kanthu ka mau a Yehova, amene Yehova ananena za nyumba ya Ahabu; pakuti Yehova wachita chimene adanena mwa mtumiki wake Eliya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Dziŵani tsono kuti mau a Chauta, amene adanena za banja la Ahabu, sadzapita padera. Ndi Chauta amene wachitadi zimene adalankhula kudzera mwa Eliya mtumiki wake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma dziwani tsono, kuti mawu amene Yehova anayankhula kunena za banja la Ahabu sadzapita padera. Yehova wachita chimene analonjeza kudzera mwa mtumiki wake Eliya.”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 10:10
13 Mawu Ofanana  

Ndipo uzilankhula naye, ndi kuti, Atero Yehova, Kodi wapha, nulandanso? Nulankhulenso naye, kuti, Atero Yehova, Paja agalu ananyambita mwazi wa Naboti pompaja agalu adzanyambita mwazi wako, inde wako.


Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake.


Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.


Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.


Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;


Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.


Koma mau anga ndi malemba anga, amene ndinalamulira atumiki anga aneneriwo, kodi sanawapeze makolo anu? Ndipo anabwera, nati, Monga umo Yehova wa makamu analingirira kutichitira ife, monga mwa njira zathu ndi monga mwa machitidwe athu, momwemo anatichitira.


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.


Ndipo Samuele anakula, Yehova nakhala naye, osalola kuti mau ake amodzi apite pachabe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa