Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:17 - Buku Lopatulika

17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m'malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Motero Ahaziya adafadi potsata mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Eliya. Ndipo popeza kuti Ahaziya adaalibe mwana wamwamuna, Yoramu mbale wake adaloŵa ufumu m'malo mwake, pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehoramu, mwana wa Yosafati, mfumu ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula. Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:17
11 Mawu Ofanana  

Mbiya ya ufa siidathe, ndi nsupa ya mafuta siinachepe, monga mwa mau a Yehova amene ananenetsa Eliya.


Ndipo potsuka galetayo pa thawale la ku Samariya agalu ananyambita mwazi wake, paja pamasamba akazi adama, monga mwa mau a Yehova amene ananenawo.


Yehosafati anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu, pamene analowa ufumu, nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu mu Yerusalemu. Ndi dzina la amake linali Azuba mwana wa Sili.


Ahaziya mwana wa Ahabu anayamba kukhala mfumu ya Israele pa Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yehosafati mfumu ya Yuda; nakhala mfumu ya Israele zaka ziwiri.


Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwe kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?


Ndipo anafika ku Samariya, nakantha onse otsala a Ahabu mu Samariya, mpaka adamuononga monga mwa mau a Yehova adanenawo kwa Eliya.


Ndipo Yehoramu mwana wa Ahabu analowa ufumu wa Israele mu Samariya m'chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yehosafati mfumu ya Yuda, nakhala mfumu zaka khumi ndi ziwiri.


Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;


Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.


Ndipo Mose mtumiki wa Yehova anamwalirako m'dziko la Mowabu, monga mwa mau a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa