2 Mafumu 1:16 - Buku Lopatulika16 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Ndipo Eliya adauza mfumuyo kuti “Chauta akunena kuti, ‘Pamene udaatuma amithenga kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, kodi ndiye kuti kuno ku Israele kulibe Mulungu woti nkumpempha nzeru?’ Nchifukwa chake Chauta akuti, ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ” Onani mutuwo |
Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.