Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 1:14 - Buku Lopatulika

14 Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Onani, moto udatsika kumwamba nupsereza anzanga aja, pamodzi ndi anthu ao omwe. Chonde tipulumutseni, musatiwononge.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Taonani, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kupsereza atsogoleri awiri pamodzi ndi anthu awo onse. Koma tsopano musawononge moyo wanga!”

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 1:14
11 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.


Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu.


Imfa ya okondedwa ake nja mtengo wake pamaso pa Yehova.


Popeza chiombolo cha moyo wao ncha mtengo wake wapatali, ndipo chilekeke nthawi zonse.


Adzaombola moyo wao ku chinyengo ndi chiwawa; ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pake.


Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.


Komatu sindiuyesa kanthu moyo wanga, kuti uli wa mtengo wake kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kuchitira umboni Uthenga Wabwino wa chisomo cha Mulungu.


Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.


Ndipo onani, monga lero ndinasamalira ndithu moyo wanu, momwemo usamaliridwe ndithu moyo wanga pamaso pa Yehova, ndipo Iye andipulumutse ku masautso onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa