Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 5:10 - Buku Lopatulika

10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirire umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; iye wosakhulupirira Mulungu anamuyesa Iye wonama; chifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anauchita wa Mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu, ali nawo umboniwo mumtima mwake. Amene sakhulupirira Mulungu, amayesa kuti Mulungu ndi wonama, chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu adachitira Mwana wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 5:10
22 Mawu Ofanana  

Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza, ndi kuyesa mau anga opanda pake?


Chinsinsi cha Yehova chili kwa iwo akumuopa Iye; ndipo adzawadziwitsa pangano lake.


Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka.


Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani?


Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?


Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?


Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


Wokhulupirira Iye saweruzidwa; wosakhulupirira waweruzidwa ngakhale tsopano, chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.


Iye amene analandira umboni wake anaikapo chizindikiro chake kuti Mulungu ali woona.


Ndipo mulibe mau ake okhala mwa inu; chifukwa kuti amene Iyeyu anatuma, inu simumkhulupirira ameneyo.


Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;


Koma ndinena kuti, pokhala wolowa nyumba ali wakhanda, sasiyana ndi kapolo, angakhale ali mwini zonse;


Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!


Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Ndipo tili nao mau a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m'malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu;


Tikanena kuti sitidachimwe, timuyesa Iye wonama, ndipo mau ake sakhala mwa ife.


Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, ndipo chinachoka kunka kuchita nkhondo ndi otsala a mbeu yake, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


ndipo ndidzampatsa iye nthanda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa