Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 3:6 - Buku Lopatulika

6 Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuone Iye, ndipo sanamdziwe Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Yense wakukhala mwa Iye sachimwa; yense wakuchimwa sanamuona Iye, ndipo sanamdziwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Munthu aliyense wokhala mwa Khristu, sachimwa. Aliyense amene amachimwa, sadamuwone ndipo sadamdziŵe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 3:6
11 Mawu Ofanana  

Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.


Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.


Ndipo tsopano, tiana, khalani mwa Iye; kuti akaonekere Iye tikakhale nako kulimbika mtima, osachita manyazi kwa Iye pa kudza kwake.


Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.


Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;


Okondedwa, tsopano tili ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Tidziwa kuti, pa kuoneka Iye, tidzakhala ofanana ndi Iye, Pakuti tidzamuona Iye monga ali.


Yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachita tchimo, chifukwa mbeu yake ikhala mwa iye; ndipo sangathe kuchimwa, popeza wabadwa kuchokera mwa Mulungu.


Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu; iye wakuchita choipa sanamuone Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa