Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:22 - Buku Lopatulika

22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Wabodza ndani, koma iye wokanayo kuti Yesu siali Khristu? Iye ndiye wokana Khristu, amene akana Atate ndi Mwana.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Wabodzayo ndani? Kodi si amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi wolonjezedwa uja? Wokana Atate ndi Mwana, ameneyo ndiye Woukira Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:22
14 Mawu Ofanana  

chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.


Pakuti ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Khristu, nadzasokeretsa anthu ambiri.


Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.


Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;


Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.


Yense wakukana Mwana, alibe Atate; wovomereza Mwana ali ndi Atatenso.


Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;


Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.


ndipo mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu suchokera kwa Mulungu; ndipo uwu ndiwo mzimu wa wokana Khristu umene mudamva kuti ukudza; ndipo ulimo m'dziko lapansi tsopano lomwe,


Yense wokhulupirira kuti Yesu ndiye Khristu wabadwa kuchokera kwa Mulungu; ndipo yense wakukonda Iye amene anabala akondanso iye amene anabadwa wochokera mwa Iye.


Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.


Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa