Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Timoteyo 6:3 - Buku Lopatulika

3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ngati munthu aphunzitsa zina, wosavomerezana nao mau a moyowo a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chiphunzitsocho chili monga mwa chipembedzo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu,

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 6:3
19 Mawu Ofanana  

Kuchiza lilime ndiko mtengo wa moyo; koma likakhota liswa moyo.


Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;


Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,


zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pake;


Gwira chitsanzo cha mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:


Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo,


wogwira mau okhulupirika monga mwa chiphunzitso, kuti akakhoze kuchenjeza m'chiphunzitso cholamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.


Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a ntchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa