Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Timoteyo 1:7 - Buku Lopatulika

7 pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a Malamulo a Mulungu, chonsecho samvetsa zimene iwo omwe akunena kapena zimene akufuna kutsimikiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 1:7
20 Mawu Ofanana  

Kawalekeni iwo, ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m'mbuna.


Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, Inenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizichita izi.


Ndipo pakupita masiku atatu, anampeza Iye mu Kachisi, analikukhala pakati pa aphunzitsi, namva iwo, nawafunsanso mafunso.


Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapanda kudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.


Pakunena kuti ali anzeru, anapusa;


Ichi chokha ndifuna kuphunzira kwa inu, Kodi munalandira Mzimuyo ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?


Ndipo iye amene akuonjezerani inu Mzimuyo, nachita zimphamvu mwa inu, atero kodi ndi ntchito za lamulo, kapena ndi kumva kwa chikhulupiriro?


Ndiuzeni, inu akufuna kukhala omvera lamulo, kodi simukumva chilamulo?


iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;


ophunzira nthawi zonse, koma sangathe konse kufikira kuchizindikiritso cha choonadi.


Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.


Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa