Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 25:31 - Buku Lopatulika

31 mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 mudzakhala opanda chakudodoma nacho, kapena chakusauka nacho mtima wa mbuye wanga, chakuti munakhetsa mwazi wopanda chifukwa, kapena kuti mbuye wanga anabwezera chilango ndipo Yehova akadzachitira mbuye wanga zabwino, pamenepo mukumbukire mdzakazi wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Nthaŵi imeneyo inu simudzamva chisoni kapena kuvutika mu mtima kuti mudakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Ndipo pamene Chauta adzakuchitirani zabwino zonsezi, musadzandiiŵale ine mdzakazi wanu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:31
13 Mawu Ofanana  

Koma undikumbukire ine m'mene kudzakhala bwino ndi iwe, ndipo undichitiretu ine kukoma mtima: nunditchule ine kwa Farao, nunditulutse ine m'nyumbamu:


inde Mulungu wakundibwezera chilango ine, ndi kundigonjetsera anthu a mitundu.


Mulungu wakubwezera chilango, Yehova, Mulungu wakubwezera chilango, muoneke wowala.


Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m'mene mulowa Ufumu wanu.


Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.


Kuli kwabwino kusadya nyama, kapena kusamwa vinyo, kapena kusachita chinthu chilichonse chakukhumudwitsa mbale wako.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Chifukwa chake Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, nandigwirire moyo, nandipulumutse m'dzanja lanu.


Ndipo kudzali, pamene Yehova anachitira mbuye wanga monga mwa zabwino zonse adalankhula za inu, ndipo adadzaika inu mukhale kalonga wa Israele;


ndipo, kudalitsike kuchenjera kwako, nudalitsike iwe, pakuti unandiletsa kusakhetsa mwazi, ndi kusabwezera chilango ndi dzanja la ine ndekha.


Ndipo anyamata a Davide pakufika kwa Abigaile ku Karimele, analankhula naye, nati, Davide anatitumiza kwa inu, kukutengani, mukhale mkazi wake.


Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa