Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 25:28 - Buku Lopatulika

28 Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Chonde, mukhululukire cholakwa cha ine mdzakazi wanu. Zoonadi, Chauta adzakhazikitsa banja lanu mu ufumu, poti mukummenyera nkhondo. Motero choipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:28
31 Mawu Ofanana  

Masiku anapitawo, pamene Saulo anali mfumu yathu, inu ndinu amene munatsogolera Aisraele kutuluka nao ndi kubwera nao; ndipo Yehova ananena nanu, Uzidyetsa anthu anga Israele, ndi kukhala mtsogoleri wa Israele.


monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.


Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.


Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, munawulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; chifukwa chake mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero ili kwa Inu.


Nayenda iye m'zoipa zonse za atate wake, zimene iye adachita asanalowe ufumu Abiyayo; ndipo mtima wake sunali wangwiro ndi Yehova Mulungu wake monga mtima wa Davide kholo lake.


chifukwa kuti Davide adachita cholungama pamaso pa Yehova, osapatuka masiku ake onse pa zinthu zonse adamlamulira Iye, koma chokhacho chija cha Uriya Muhiti.


pamenepo Ine ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wako pa Israele nthawi yosatha, monga ndinalonjezana ndi Davide atate wako, ndi kuti, Sadzakusowa munthu wamwamuna pa mpando wachifumu wa Israele.


ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israele; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.


Pakuti Inu, Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzammangira banja; momwemo mtumiki wanu waona mtima wakupemphera pamaso panu.


nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala mu Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.


Yehova Mulungu wanga, ngati ndachita ichi; ngati m'manja anga muli chosalungama;


Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba.


Sayang'anira mphulupulu ili mu Yakobo, kapena sapenya kupulukira kuli mu Israele. Yehova Mulungu wake ali ndi iye, ndi mfuu wa mfumu uli pakati pao.


Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.


Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachite kanthu kolakwa.


Ndipo pamene kenturiyo anaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.


Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang'amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.


Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo Iye adzakuperekani inu m'manja athu.


Ndipo Saulo anati kwa Davide, Ona, mwana wanga wamkazi wamkulu, dzina lake Merabi, iyeyo ndidzakupatsa akhale mkazi wako; koma undikhalire ngwazi, nuponye nkhondo za Yehova. Pakuti Saulo anati, Dzanja langa lisamkhudze, koma dzanja la Afilisti ndilo.


Ndipo ndidzadziukitsira wansembe wokhulupirika, amene adzachita monga chimene chili mumtima mwanga ndi m'chifuniro changa; ndipo ndidzammangira nyumba yokhazikika, ndipo iyeyu adzayenda pamaso pa wodzozedwa wanga masiku onse.


Ndipo Ahimeleki anayankha mfumu, nati, Ndipo ndani mwa anyamata anu onse ali wokhulupirika ngati Davide amene, mkamwini wa mfumu; wakuyenda mu uphungu wanu, nalemekezeka m'nyumba mwanu?


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.


Chifukwa chake tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.


Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.


Ndipo atagwadira pa mapazi ake anati, Pa ine, mbuye wanga, pa ine pakhale uchimowo; ndipo mulole mdzakazi wanu alankhule m'makutu anu, nimumvere mau a mdzakazi wanu.


Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa