Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 25:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo mphatso iyi mdzakazi wanu ndatengera mbuye wanga, ipatsidwe kwa anyamata akutsata mbuye wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Pepani, nazi mphatsozi zimene mdzakazi wanune ndabwera nazo kwa inu mbuyanga, kuti zipatsidwe kwa anthu muli nawoŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Choncho, nazi mphatso zimene mdzakazi wanu ndabwera nazo kwa mbuye wanga kuti zipatsidwe kwa anyamata amene muli nawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 25:27
8 Mawu Ofanana  

Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindikwanira. Ndipo anamkakamiza, nalandira.


Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko.


Pamenepo anabwerera kwa munthu wa Mulungu iye ndi gulu lake lonse, nadzaima pamaso pake, nati, Taonani, tsopano ndidziwa kuti palibe Mulungu padziko lonse lapansi, koma kwa Israele ndiko; ndipo tsopano, mulandire chakukuyamikani nacho kwa mnyamata wanu.


Mtulo wa munthu umtsegulira njira, numfikitsa pamaso pa akulu.


Chifukwa chake ndinayesa kuti kufunika kupempha abale kuti atsogole afike kwa inu, nakonzeretu dalitso lanu lolonjezeka kale, kuti chikhale chokonzeka chomwechi, monga ngati mdalitso, ndipo si monga mwa kuumiriza.


Ndipo Baraki anaitana Zebuloni ndi Nafutali asonkhane ku Kedesi; iye nakwera ndi anthu zikwi khumi akumtsata; Deboranso anakwera kunka naye.


Ndipo Abigaile anafulumira nanyamuka, nakwera pabulu, pamodzi ndi anamwali ake asanu akumtsata; natsatira mithenga ya Davide, nakhala mkazi wake.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa