Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 9:2 - Buku Lopatulika

2 Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'mizinda mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Antchito a m'kachisi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Okhala m'dziko oyamba tsono, akukhala mwaomwao m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, Alevi, ndi Anetini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Aisraele oyamba kukakhala m'maiko mwao ndi m'mizinda yao anali anthu wamba, ansembe, Alevi ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 9:2
11 Mawu Ofanana  

Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:


Antchito a m'kachisi: ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,


Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.


Ndipo ansembe, ndi Alevi, ndi anthu ena, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, anakhala m'midzi mwao, ndi Aisraele onse m'midzi mwao.


ndi antchito a m'kachisi, amene Davide ndi akalonga adapereka atumikire Alevi, antchito a m'kachisi mazana awiri mphambu makumi awiri, onsewo otchulidwa maina.


amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;


Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.


Antchito onse a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni, ndiwo mazana atatu mphambu makumi asanu ndi anai kudza awiri.


Nakhala m'midzi mwao ansembe, ndi Alevi, ndi odikira, ndi oimbira, ndi anthu ena, ndi antchito a m'kachisi, ndi Aisraele onse. Utakhala tsono mwezi wachisanu ndi chiwiri ana a Israele anakhala m'midzi mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa