Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 9:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Aisraele onse anawerengedwa mwa chibadwidwe chao; ndipo taonani, alembedwa m'buku la mafumu a Israele; ndipo Yuda anatengedwa ndende kunka ku Babiloni chifukwa cha kulakwa kwao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Tsono Aisraele onse adalembedwa potsata mibadwo yao m'buku la mafumu a Aisraele. Anthu a ku Yuda adaatengedwa ukapolo kunka ku Babiloni chifukwa chakuti anali osakhulupirika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli. Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 9:1
22 Mawu Ofanana  

Ndipo machitidwe ena a Yerobowamu m'mene umo anachitira ufumu, taona, analembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.


Nachoka nao a mu Yerusalemu onse, ndi akalonga onse, ndi ngwazi zonse, ndiwo andende zikwi khumi, ndi amisiri onse, ndi osula onse; sanatsale ndi mmodzi yense, koma anthu osauka okhaokha a m'dziko.


Nachoka naye Yehoyakini kunka naye ku Babiloni, ndi make wa mfumu, ndi akazi a mfumu, ndi adindo ake, ndi omveka a m'dziko; anachoka nao andende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni.


Ndi anthu amphamvu onse, ndiwo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi amisiri, ndi osula chikwi chimodzi, onsewo achamuna oyenera nkhondo, omwewo mfumu ya Babiloni anadza nao andende ku Babiloni.


Ndipo ana a Ulamu ndiwo ngwazi zamphamvu, ndiwo oponya mivi, nakhala nao ana ambiri ndi zidzukulu zana limodzi. Onsewa ndiwo a ana a Benjamini.


Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asiriya, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babiloni.


Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:


Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:


Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.


Ndipo Mulungu wanga anaika m'mtima mwanga kuti ndiwasonkhanitse aufulu, ndi olamulira, ndi anthu, kuti awerengedwe mwa chibadwidwe chao. Ndipo ndinapeza buku la chibadwidwe la iwo adakwerako poyamba paja; ndinapeza mudalembedwa m'mwemo.


Awa anafunafuna maina ao m'buku la iwo owerengedwa mwa chibadwidwe, koma osawapeza; potero anawayesa odetsedwa, nawachotsa kuntchito ya nsembe.


munthu wamphamvu, ndi munthu wankhondo; woweruza ndi mneneri, ndi waula, ndi nkhalamba;


Mizinda ya kumwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda yense wachotsedwa m'ndende yenseyo, wachotsedwa m'nsinga.


Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga anthu otsalira m'mzinda, ndi othawa omwe, opandukira, ndi kumtsata ndi anthu otsalira nanka nao am'nsinga ku Babiloni.


Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa