Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 6:71 - Buku Lopatulika

71 Ana a Geresomo analandira motapa pa mabanja a hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndi Asitaroti ndi mabusa ake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

71 Ana a Geresomo analandira motapa pa mabanja a fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndi Asitaroti ndi mabusa ake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

71 Mizinda yochokera pa fuko la Manase wakuvuma, imene Ageresomo adalandira, ndi iyi: Golani ku Basani pamodzi ndi mabusa ake omwe ndiponso Asitaroti pamodzi ndi mabusa ake omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

71 Ageresomu analandira malo awa: Kuchokera ku theka la fuko la Manase, analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto;

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 6:71
9 Mawu Ofanana  

ndi motapa pa hafu la fuko la Manase, Anere ndi mabusa ake, ndi Bileamu ndi mabusa ake, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.


ndi motapa pa fuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake,


atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.


ndiyo Bezeri, m'chipululu, m'dziko lachidikha, ndiwo wa Arubeni; ndi Ramoti mu Giliyadi, ndiwo wa Agadi; ndi Golani, mu Basani, ndiwo wa Amanase.


ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.


Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti mu Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani mu Basani wa fuko la Manase.


Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa hafu la fuko la Manase, Golani mu Basani ndi mabusa ake, ndiwo mzinda wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; mizinda iwiri.


Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa hafu la fuko la Manase mu Basani, mizinda khumi ndi itatu.


ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa