Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 6:3 - Buku Lopatulika

3 Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ana a Amuramu naŵa: Aroni, Mose ndi Miriyamu. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abibu, Eleazara ndi Itamara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ana a Amramu anali awa: Aaroni, Mose ndi Miriamu. Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 6:3
18 Mawu Ofanana  

a ana a Uziyele, Aminadabu mkulu wao, ndi abale ake zana limodzi mphambu khumi ndi awiri.


Ana a Kohati: Amuramu, Izihara, Hebroni, ndi Uziyele; anai.


Ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose; ndipo Aroni anasankhidwa kuti apatule zopatulika kwambiri, iye ndi ana ake, kosalekeza, kufukiza pamaso pa Yehova, kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kosatha.


Wa Aizihara: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.


Ndi ana a Kohati: Amuramu, Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.


Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,


Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.


Ndipo mlongo wake anaima patali, adziwe chomwe adzamchitira.


Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?


Ndipo Iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akulu a Israele makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;


Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ake aamuna pamodzi naye, mwa ana a Israele, kuti andichitire Ine ntchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara, ana a Aroni.


Ndipo Amuramu anadzitengera Yokebede mlongo wa atate wake akhale mkazi wake; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amuramu ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri.


Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Nasoni, akhale mkazi wake; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara.


Ndipo ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu anatenga yense mbale yake ya zofukiza, naikamo moto, naikapo chofukiza, nabwera nao pamaso pa Yehova moto wachilendo, umene sanawauze.


Ndipo Mose ananena ndi Aroni, ndi Eleazara ndi Itamara, ana ake otsala, Tengani nsembe yaufa yotsalira ku nsembe zamoto za Yehova, ndi kuidya yopanda chotupitsa pafupi paguwa la nsembe; pakuti ndiyo yopatulika kwambiri;


Ndipo Mose anafunafuna mbuzi ya nsembe yauchimo, ndipo taonani, adaitentha. Ndipo anapsa mtima pa Eleazara ndi Itamara, ana otsalawo a Aroni, nati,


Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa