Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 5:6 - Buku Lopatulika

6 Beera mwana wake, amene Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Beera mwana wake, amene Tigilati-Pilesere mfumu ya ku Asiriya anamtenga ndende; ndiye kalonga wa Arubeni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 ndi Beera amene Tigilati-Pilesere, mfumu ya ku Asiriya, idamtenga ukapolo. Iyeyo anali mmodzi mwa atsogoleri a Arubeni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 5:6
6 Mawu Ofanana  

Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.


Ndipo Ahazi anatuma mithenga kwa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndi kuti, Ine ndine kapolo wanu ndi mwana wanu; kwerani, mudzandipulumutse m'dzanja la mfumu ya Aramu, ndi m'dzanja la mfumu ya Israele anandiukirawo.


Ndipo Mulungu wa Israele anautsa mzimu wa Pulo mfumu ya Asiriya, ndi mzimu wa Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, ndiye anawatenga ndende; ndiwo Arubeni, ndi Agadi, ndi hafu la fuko la Manase, nafika nao ku Hala, ndi Habori, ndi Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, mpaka lero lino.


Mika mwana wake, Reaya mwana wake, Baala mwana wake,


Ndi abale ake monga mwa mabanja ao, powerenga chibadwidwe cha mibadwo yao: akulu ndiwo Yeiyele, ndi Zekariya,


Ndipo Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa