Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 3:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo mwana wa Solomoni ndiye Rehobowamu, Abiya mwana wake, Asa mwana wake, Yehosafati mwana wake,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Nazi zidzukulu za Solomoni: Rehobowamu adabereka Abiya, Abiya adabereka Asa, Asa adabereka Yehosafati,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa, Asa anabereka Yehosafati,

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 3:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anagona ndi makolo ake, naikidwa m'mzinda wa Davide atate wake; ndipo Rehobowamu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


Nagona Rehobowamu ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide. Ndipo dzina la amake linali Naama Mwamoni, nalowa ufumu m'malo mwake Abiya mwana wake.


Nagona Asa ndi makolo ake, naikidwa kwa makolo ake m'mzinda wa Davide kholo lake; ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu m'malo mwake.


Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wake.


Nagona Abiya ndi makolo ake, namuika anthu m'mzinda wa Davide; Asa mwana wake nalowa ufumu m'malo mwake.


Yoramu mwana wake, Ahaziya mwana wake, Yowasi mwana wake,


Onsewa ndiwo ana a Davide, pamodzi ndi ana a akazi aang'ono; ndipo Tamara ndiye mlongo wao.


Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yerobowamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.


Momwemo Abiya anagona ndi makolo ake, ndipo anamuika m'mzinda wa Davide; ndi Asa mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake; m'masiku ake dziko linaona bata zaka khumi.


Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa