Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 27:5 - Buku Lopatulika

5 Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m'chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Kazembe wachitatu wa khamu wa mwezi wachitatu ndiye Benaya mwana wa Yehoyada wansembe wamkulu; ndi m'chigawo mwake munalinso zikwi makumi awiri mphambu zinai.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mtsogoleri wa ankhondo pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa Yehoyada mkulu wa ansembe. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 27:5
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.


Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.


ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lake akulu makumi awiri mphambu awiri.


ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.


ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.


Woyang'anira chigawo cha mwezi wachiwiri ndiye Dodai Mwahohi ndi chigawo chake; ndi Mikiloti mtsogoleri, ndi m'chigawo chake munali zikwi makumi awiri mphambu zinai.


Benaya ameneyo ndiye wamphamvu uja wa makumi atatu aja, woyang'anira chigawo chake ndi Amizabadi mwana wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa