1 Mbiri 27:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo ana a Israele monga mwa chiwerengo chao, kunena za akulu a nyumba za makolo ao, ndi akazembe a zikwi, ndi a mazana, ndi akapitao ao akutumikira mfumu mu ntchito iliyonse ya magawidwe, akulowa ndi kutuluka mwezi ndi mwezi, miyezi yonse ya chaka, chigawo chilichonse ncha amuna zikwi makumi awiri mphambu zinai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Nawu mndandanda wa atsogoleri a mabanja a Aisraele olamulira ankhondo zikwi ndiponso ankhondo mazana, pamodzi ndi akulu ao amene ankatumikira mfumu. Ankasinthanasinthana mwezi ndi mwezi pa chaka chilichonse, gulu lililonse linali ndi anthu okwanira 24,000. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000. Onani mutuwo |
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.