Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 26:1 - Buku Lopatulika

1 A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 A magawidwe a odikira a Akora: Meselemiya mwana wa Kore wa ana a Asafu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Magulu a alonda odikira pa khomo naŵa: m'gulu la Akora munali Meselemiya, mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Magulu a alonda a pa zipata: Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 26:1
15 Mawu Ofanana  

ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwachiwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaaziele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, Eliyabu, ndi Benaya, ndi Maaseiya, ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, odikirawo.


ndi zikwi zinai odikira; ndi zikwi zinai analemekeza Yehova ndi zoimbira zimene ndinazipanga, anati Davide, kuti alemekeze nazo.


wa makumi awiri ndi chinai Romamiti-Ezere, ana ake ndi abale ake khumi ndi awiri.


Ndipo Meselemiya anali ndi ana, woyamba Zekariya, wachiwiri Yediyaele, wachitatu Zebadiya, wachinai Yatiniele,


Ndi Meselemiya anali ndi ana, ndi abale odziwa mphamvu khumi mphambu asanu ndi atatu.


mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora,


Ndi a Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, a ana a Merari;


Ndipo anaika odikira kumakomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kalikonse asalowemo.


Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.


Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.


Dzamveni kuno, anthu inu nonse; tcherani khutu, inu nonse amakono,


Koma adzakhala atumiki m'malo anga opatulika, akuyang'anira kuzipata za Kachisi, ndi kutumikira mu Kachisimo, aziwaphera anthu nsembe yopsereza, ndi nsembe yophera, naime pamaso pao kuwatumikira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa