1 Mbiri 24:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo anapeza kuti amuna aakulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo anapeza kuti amuna akulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Popeza kuti pakati pa zidzukulu za Eleazara padapezeka atsogoleri ambiri kupambana pakati pa zidzukulu za Itamara, Davide adasankhula atsogoleri 16 pakati pa zidzukulu za Eleazara, ndiponso asanu ndi atatu pakati pa zidzukulu za Itamara. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. Onani mutuwo |