1 Mbiri 24:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao mu utumiki wao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao m'utumiki wao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Zidzukulu za Aroni mfumu Davide adazigaŵira ntchito molongosoka bwino, pothandizidwa ndi Zadoki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. Onani mutuwo |
Ndipo anaika monga mwa chiweruzo cha Davide atate wake zigawo za ansembe ku utumiki wao, ndi Alevi ku udikiro wao, kulemekeza Mulungu, ndi kutumikira pamaso pa ansembe, monga munayenera tsiku ndi tsiku; odikira omwe monga mwa zigawo zao ku chipata chilichonse; pakuti momwemo Davide munthu wa Mulungu adamuuza.