1 Mbiri 22:3 - Buku Lopatulika3 Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Nakonzeratu Davide chitsulo chochuluka cha misomali ya ku zitseko za zipata, ndi ya kuphatikizitsa; ndi mkuwa wochuluka wosauyesa kulemera kwake; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Davide adaperekanso zitsulo zochuluka zopangira misumali ya zitseko zapamakomo ndi nsimbi zomangira. Adaperekanso mkuŵa wochuluka, wokanika kuuyesa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza. Onani mutuwo |
Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka.