Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 22:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Davide anati asonkhanitse alendo okhala m'dziko la Israele; iye naika osema miyala afukule miyala, aiseme kuti amange nayo nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Davide adalamula kuti asonkhanitse alendo amene anali m'dziko la Israele. Tsono pakati pao adasankhula anthu oti aseme miyala yomangira Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Choncho Davide analamula kuti asonkhanitse alendo onse amene amakhala mu Israeli ndipo kuchokera pakati pawo anasankha amisiri a miyala kuti aseme miyala yomangira nyumba ya Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 22:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Hiramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide ndi mitengo yamkungudza, ndi amisiri a matabwa, ndi omanga nyumba; iwo nammangira Davide nyumba.


Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m'nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.


ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.


kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.


Ndipo Huramu mfumu ya Tiro anatumiza mithenga kwa Davide, ndi mikungudza, ndi amisiri omanga miyala, ndi amatabwa, kuti ammangire nyumba.


Mfumu Davide ananenanso kwa khamu lonse, Mulungu wasankha mwana wanga Solomoni yekha, ndiye mnyamata ndi wosakhwima; ndipo ntchitoyi ndi yaikulu, pakuti chinyumbachi sichili cha munthu, koma cha Yehova Mulungu.


ndipo ife tidzatema mitengo ku Lebanoni monga mwa kusowa kwanu konse; ndipo tidzabwera nayo kwa inu yoyandamitsa paphaka kufikira ku Yopa; ndipo inu mudzakwera nayo ku Yerusalemu.


Ndipo Solomoni anawerenga alendo onse okhala m'dziko la Israele, monga mwa mawerengedwe aja atate wake Davide adawawerenga nao, nawapeza afikira zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu kudza zitatu ndi mazana asanu ndi limodzi.


Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.


kuti nthawi ija munali opanda Khristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israele, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa