Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 22:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Davide anati, Pano padzakhala nyumba ya Yehova Mulungu, ndi pano padzakhala guwa la nsembe yopsereza la Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Davide adati, “Pano ndipo pamene padzakhale Nyumba ya Mulungu, ndiponso pano mpamene padzakhale guwa la nsembe zopsereza zimene Aisraele azidzapereka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ndipo Davide anati, “Nyumba ya Yehova Mulungu idzakhala pano, ndiponso guwa lansembe zopsereza za Israeli.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 22:1
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anaopa, nati, Poopsa pompano! Pompano ndipo pa nyumba ya Mulungu, si penai, pompano ndipo pa chipata cha kumwamba.


Ndipo Gadi anafika tsiku lomwelo kwa Davide nanena naye, Kwerani mukamangire Yehova guwa la nsembe pa dwale la Arauna Myebusi.


Ndipo mukati kwa ine, Tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; sindiye amene Hezekiya wamchotsera misanje yake ndi maguwa a nsembe ake, nati kwa Yuda ndi kwa Yerusalemu, Muzilambira paguwa la nsembe pano mu Yerusalemu?


Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.


Pamenepo Solomoni anayamba kumanga nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, m'phiri la Moriya, kumene Mulungu anaonekera kwa Davide atate wake pamalo pamene Davide anakonzeratu pa dwale la Orinani Myebusi.


Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?


ndipo anachokera chokhalamo cha ku Silo, chihemacho adachimanga mwa anthu;


Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


koma pamalo pamene Yehova adzasankha, mwa limodzi la mafuko anu, pamenepo muzipereka nsembe zanu zopsereza, ndi pamenepo muzichita zonse ndikuuzani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa