Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 21:3 - Buku Lopatulika

3 Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma Yowabu adati, “Chauta achulukitse pa chiwerengero anthu ake makumi khumi kupambana m'mene alirimu. Kodi anthu onseŵa mbuyanga mfumu si atumiki anu? Nanga chifukwa chiyani mbuyanga akufuna zimenezi? Chifukwa chiyani akufuna kuchimwitsa Aisraele?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 21:3
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu, nati kwa iye, Watichitira ife chiyani iwe? Ndakuchimwiranji iwe kuti waufikitsa pa ine ndi pa ufumu wanga uchimo waukulu? Wandichitira ine zosayenera kuzichita.


Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.


Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.


Limbika mtima, tilimbikire anthu athu, ndi mizinda ya Mulungu wathu; ndipo Yehova achite chomkomera.


Koma mau a mfumu anamtsutsa Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza ku Yerusalemu.


Yehova akuonjezereni dalitso, inu ndi ana anu.


Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?


Mu unyinji wa anthu muli ulemu wa mfumu; koma popanda anthu kalonga aonongeka.


Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.


mbeu yakonso ikadakhala monga mchenga, ndi obadwa a m'chuuno mwako momwemo; dzina lake silikadachotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.


Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu!


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa