1 Mbiri 20:3 - Buku Lopatulika3 Natulutsanso anthu anali m'mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi mizinda yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Natulutsanso anthu anali m'mwemo, nawacheka ndi mipeni ya manomano, ndi zipangizo zochekera zachitsulo, ndi nkhwangwa. Anatero Davide ndi midzi yonse ya ana a Amoni. Ndipo Davide ndi anthu onse anabwera ku Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Adaŵatulutsa anthu amumzindamo, nakaŵagwiritsa ntchito ndi masowo, zikumbiro zachitsulo ndi nkhwangwa. Umu ndimo m'mene Davide adachitira ndi mizinda yonse ya Aamoni. Pambuyo pake Davideyo adabwerera ku Yerusalemu pamodzi ndi ankhondo onse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka Davide pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu. Onani mutuwo |