Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndi ana a Karimi: Akara wovuta Israeleyo, amene analakwira choperekedwa chiperekerecho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ana a Karimi naŵa: Akara amene adaavuta Aisraele. Iyeyo adaaba zinthu zoyenera kuziwononga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 2:7
10 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Zera: Zimiri, ndi Etani, ndi Hemani, ndi Kalikoli, ndi Dara; onse pamodzi ndi asanu.


Ndi mwana wa Etani: Azariya.


Ana a Yuda: Perezi, Hezironi, ndi Karimi, ndi Huri, ndi Sobala.


Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;


Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.


Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwe m'choperekedwacho, ndipo mkwiyo unagwera gulu lonse la Israele? Osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yake.


Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa.


Ndipo Yoswa anati, Watisautsiranji? Yehova adzakusautsa lero lino. Ndipo Aisraele onse anamponya miyala, nawatentha ndi moto, nawaponya miyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa