Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 2:23 - Buku Lopatulika

23 Ndi Gesuri ndi Aramu analanda mizinda ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi midzi yake; ndiyo mizinda makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndi Gesuri ndi Aramu analanda midzi ya Yairi, pamodzi ndi Kenati ndi milaga yake; ndiyo midzi makumi asanu ndi limodzi. Iwo onse ndiwo ana a Makiri atate wa Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Koma anthu a ku Gesuri ndi a ku Aramu adaŵalanda Havoti-Yairi, Kenati pamodzi ndi midzi yake yomwe, yonse pamodzi inalipo midzi 60. Onseŵa anali adzukulu a Makiri, bambo wake wa Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 2:23
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.


Chomwecho anathawa Abisalomu, nanka ku Gesuri, nakakhala kumeneko zaka zitatu.


Benigebere ku Ramoti Giliyadi, iyeyo anali nayo mizinda ya Yairi mwana wa Manase ili mu Giliyadiyo, iye anali nalo dziko la Arigobu lili mu Basani, mizinda yaikulu makumi asanu ndi limodzi yamalinga ndi zitseko zamkuwa;


Ndi Segubu anabala Yairi, amene anali nayo mizinda makumi awiri mphambu itatu m'dziko la Giliyadi.


Ndipo atafa Hezironi mu Kalebe-Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anambalira Asiriya atate wa Tekowa.


Yairi mwana wa Manase analanda dziko lonse la Arigobu, kufikira malire a Agesuri ndi Amaakati; nalitcha dzina lake, Basani Havoti-Yairi, kufikira lero lino).


Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino.


Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi mizinda yonse ya Yairi, yokhala mu Basani, mizinda makumi asanu ndi limodzi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa