Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 2:16 - Buku Lopatulika

16 ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Alongo ao anali Zeruya ndi Abigaile. Ana a Zeruya naŵa: Abisai, Yowabu ndi Asahele, onse pamodzi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 2:16
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anazindikira kuti mtima wa mfumu unalunjika kwa Abisalomu.


Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.


Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa mu Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?


Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.


Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.


Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.


Ozemu wachisanu ndi chimodzi, Davide wachisanu ndi chiwiri;


Ndi Abigaile anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yetere Mwismaele.


Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa