Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 19:3 - Buku Lopatulika

3 akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Koma akalonga a Aamoni adauza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti m'mene Davide watuma anthu odzakuthuzitsani mtima, ndiye kuti akulemekeza bambo wanu? Osati atumiki akewo abwera kwa inu kuti adzazinde dziko, ndipo kuti akalipenya, alilande?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?”

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 19:3
12 Mawu Ofanana  

Koma akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni mbuye wao, Kodi muganiza kuti Davide alemekeza atate wanu, popeza anakutumizirani osangalatsa? Kodi Davide sanatumize anyamata ake kwa inu, kuti ayang'ane mzindawo ndi kuuzonda ndi kuupasula?


Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,


Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka achoke.


Ndipo ana a Dani anatuma a banja lao amuna asanu a mwa iwo onse, anthu olimba mtima, a ku Zora, ndi a ku Esitaoli, kuzonda dziko ndi kufunafunamo; nanena nao, Mukani, mufunefune m'dziko. Nafika iwo ku mapiri a Efuremu kunyumba ya Mika, nagona komweko.


Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?


Ndipo Akisi anayankha nanena ndi Davide, Ndidziwa kuti pamaso panga uli wabwino, ngati mthenga wa Mulungu; koma akalonga a Afilisti anena, Iye asamuke nafe kunkhondoko.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa