Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 19:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Davide anati, Ndidzamchitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wake anandichitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wake. Pofika anyamata ake a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsono Davide adati, “Ine ndidzamchitira zabwino Hanuni mwana wa Nahasi, pakuti inenso bambo wake ankandichitira zabwino.” Choncho Davide adatuma amithenga kuti akampepese Hanuni chifukwa cha imfa ya bambo wake. Tsono atumiki a Davidewo adakafika kwa Hanuni, m'dziko la Aamoni, kuti akampepese.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa,

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 19:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anati, Kodi atsalako wina wa nyumba ya Saulo, kuti ndimchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?


Ndipo Davide ananena naye, Usaopa, pakuti zoonadi ndidzakuchitira kukoma mtima chifukwa cha Yonatani atate wako; ndi minda yonse ya Saulo ndidzakubwezera, ndipo udzadya pa gome langa chikhalire.


Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.


Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.


akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kuchitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? Sakudzerani kodi anyamata ake kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?


Tsiku lomwelo anawerenga m'buku la Mose m'makutu a anthu, napeza m'menemo kuti Aamoni ndi Amowabu asalowe mu msonkhano wa Mulungu kunthawi yonse;


Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.


Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;


Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu.


koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.


koma ambiri a mwa Ayuda adadza kwa Marita ndi Maria, kudzawatonthoza mtima pa mlongo wao.


Ndipo pamene Davide anafika ku Zikilagi, anatumizako za zofunkhazo kwa akulu a Yuda, ndiwo abwenzi ake, nati, Siyi mphatso yanu ya zofunkha za adani a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa