Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 18:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndipo Davide adalanda Hadadezere magaleta 1,000, anthu a pa akavalo 7,000, ndi asilikali apansi 20,000. Atatero, Davide adadula mitsempha ya miyendo ya akavalo onse okoka magaleta, koma adasungako akavalo okwanira magaleta 100.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 18:4
11 Mawu Ofanana  

Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa msonkhano yao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.


Ndipo Davide anatenga apakavalo ake chikwi chimodzi mphambu mazana asanu ndi awiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; ndipo Davide anadula mitsita akavalo onse a magaleta, koma anasunga a iwo akufikira magaleta zana limodzi.


Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'mizinda yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu mu Yerusalemu.


Ndipo akulu a mfumu ndi awa: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe,


Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.


Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadadezere mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.


Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.


Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.


Ndipo Yoswa anawachitira monga Yehova adamuuza: nadula akavalo ao mitsindo, natentha magaleta ao ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa