Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 18:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ku Hamati Davideyo adagonjetsanso Hadadezere mfumu ya ku Zoba, pamene inkapita kukakhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 18:3
11 Mawu Ofanana  

Tsiku lomwelo Yehova anapangana chipangano ndi Abramu, nati, Ndidzapatsa mbeu zako dziko ili, kuyambira pamtsinje wa ku Ejipito kufikira pamtsinje waukulu, mtsinje wa Yufurate:


Ndipo pamene ana a Amoni anazindikira kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, ana a Amoniwo anatumiza nadzilembera Aaramu a ku Beterehobu, ndi Aaramu a ku Zoba, oyenda pansi zikwi makumi awiri, ndi mfumu ya ku Maaka ndi anthu chikwi chimodzi, ndi anthu a mfumu ya ku Tobu zikwi khumi ndi ziwiri.


Davide anakanthanso Hadadezere, mwana wa Rehobu, mfumu ya ku Zoba, pomuka iye kukadzitengeranso ufumu wake ku chimtsinje cha Yufurate.


Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso.


Ndipo Davide analanda magaleta ake chikwi chimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magaleta, koma anasungako ofikira magaleta zana limodzi.


Ndipo Solomoni anamuka ku Hamatizoba, naugonjetsa.


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


Mwatitaya Mulungu, mwatipasula; mwakwiya; tibwezereni.


Mwagwedeza dziko, mwaling'amba. Konzani ming'alu yake; pakuti ligwedezeka.


Ndipo ndidzalemba malire ako kuyambira ku Nyanja Yofiira, kufikira ku nyanja ya Afilisti, ndi kuyambira kuchipululu kufikira ku Nyanja; popeza ndidzapereka okhala m'dzikolo m'dzanja lako, ndipo uziwaingitsa pamaso pako.


Ndipo pamene Saulo atakhazikitsa ufumu wa pa Israele, iye anaponyana ndi adani ake onse pozungulira ponse, ndi Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi Edomu ndi mafumu a Zoba, ndi Afilisti; ndipo paliponse anapotolokerapo, anawalanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa