Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 18:2 - Buku Lopatulika

2 Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Anakanthanso Mowabu; ndi Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Adagonjetsanso Amowabu, ndipo Amowabuwo adasanduka otumikira Davide, ndipo ankakhoma msonkho kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 18:2
14 Mawu Ofanana  

Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.


Ndipo akafika munthu yense ndi mtulo wake, zotengera zasiliva, ndi zotengera zagolide, ndi zovala, ndi mure, ndi zonunkhira, ndi akavalo, ndi nyuru; momwemo chaka ndi chaka.


Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yake m'manja a Afilisti.


Ndipo Davide anakantha Hadadezere mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wake ku mtsinje wa Yufurate.


Mowabu ndiye mkhate wanga; pa Edomu ndidzaponya nsapato yanga. Filistiya, fuulatu chifukwa cha ine.


Ndipo adzagudukira mapewa a Afilisti kumadzulo; pamodzi adzafunkha ana a kum'mawa; adzatambasula dzanja lao pa Edomu ndi pa Mowabu; ndipo ana a Amoni adzawamvera.


Tumizani inu anaankhosa kwa wolamulira wa dziko kuchokera ku Sela kunka kuchipululu, mpaka kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.


Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi mu Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti.


Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa