Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 17:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Ndipo ndidzaŵasankhira malo anthu anga Aisraele, ndi kuŵakhazika kumeneko, kuti akhale ku malo aoao popanda kuvutikanso. Anthu achiwawa sadzaŵazunzanso monga momwe adaachitira kale lija,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja;

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 17:9
21 Mawu Ofanana  

ndi kuyambira kuja ndinaika oweruza ayang'anire anthu anga Israele; ndipo ndagonjetsa adani ako onse. Ndikuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.


ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.


Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.


Mdani sadzamuumira mtima; ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.


Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu.


Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.


Ana ako afulumira; opasula ako ndi iwo amene anakusakaza adzachoka pa iwe.


Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.


ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.


Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso kudziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzala, osawazula iwo.


Inde, ndidzasekerera iwo kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.


mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndi siliva mwa chuma chako;


Ndipo ndidzazitulutsa mwa mitundu ya anthu, ndi kuzisonkhanitsa m'maiko, ndi kulowa nazo m'dziko lao; ndipo ndidzazidyetsa pa mapiri a Israele, patimitsinje, ndi ponse pokhala anthu m'dziko.


Ndipo adzakhala m'dziko ndinalipereka kwa Yakobo mtumiki wanga, limene anakhalamo makolo anu, ndipo adzakhala m'mwemo iwo, ndi ana ao, ndi zidzukulu zao kosatha; ndi Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri wao kosatha.


Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.


Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.


ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa