Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 17:8 - Buku Lopatulika

8 ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 ndipo ndakhala ndi iwe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndakubukitsira dzina lakunga dzina la akulu okhala padziko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 17:8
24 Mawu Ofanana  

Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.


Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.


Ndipo ndinali nawe kulikonse unamukako, ndi kuononga adani ako onse pamaso pako; ndipo ndidzamveketsa dzina lako, monga dzina la akulu ali padziko lapansi.


Pamenepo Davide anaika maboma mu Aramu wa Damasiko. Ndipo Aaramu anasanduka anthu a Davide, nabwera nayo mitulo. Ndipo Yehova anamsunga Davide kulikonse anamukako.


Ndipo ku Beta ndi ku Berotai mizinda ya Hadadezere, mfumu Davide anatenga mikuwa yambiri ndithu.


Ndipo mbiri ya Davide inabuka m'maiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse.


Ndipo ichi nchaching'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.


Ndipo Natani anati kwa Davide, Muchite zonse zili m'mtima mwanu; pakuti Mulungu ali nanu.


Chifukwa chake tsono, uzitero naye mtumiki wanga Davide, Atero Yehova wa makamu, Ndinakutenga kubusa potsata iwe nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele;


Ndipo ndaikira anthu anga Israele malo, ndi kuwaoka, kuti akhale m'malo mwao osasunthikanso; ndi ana osalungama sadzawapululanso monga poyamba paja;


Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.


Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Mundionjezere ukulu wanga, ndipo munditembenukire kundisangalatsa.


Pakuti Mulungu ndiye woweruza; achepsa wina, nakuza wina.


Iye anatsitsa mafumu pa mipando yao yachifumu, ndipo anakweza aumphawi.


Ndipo Davide anakhala wochenjera m'mayendedwe ake onse; ndipo Yehova anali naye.


Ndipo Saulo anaona, nadziwa kuti Yehova ali ndi Davide; ndi kuti Mikala mwana wa Saulo anamkonda Davide.


Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa