1 Mbiri 16:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Ndipo adaika Alevi ena kuti azitumikira ku Bokosi lachipangano la Chauta, ndiye kuti azipemphera, azithokoza ndi kumatamanda Chauta, Mulungu wa Israele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. Onani mutuwo |
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;