Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 16:3 - Buku Lopatulika

3 Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Nagwira aliyense wa Israele, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa zouma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Kenaka adagaŵira Aisraele onsewo, amuna ndi akazi, aliyense mtanda wa buledi, nthuli ya nyama ndiponso keke ya mphesa zouma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 16:3
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.


Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.


Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele.


Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula.


Nanena naonso, Mukani, mukadye zonona, mukamwe zozuna, nimumtumizire gawo lake iye amene sanamkonzeretu kanthu; chifukwa lero ndilo lopatulikira Ambuye wathu; ndipo musamachita chisoni; pakuti chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.


Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula, pakuti ndadwala ndi chikondi.


Chifukwa chake Mowabu adzakuwa chifukwa cha Mowabu, onse adzakuwa; chifukwa cha maziko a Kiri-Haresefi mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.


Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Mukanso, konda mkazi wokondedwa ndi bwenzi lake, koma wakuchita chigololo, monga Yehova akonda ana a Israele, angakhale atembenukira kumilungu ina, nakonda nchinchi za mphesa zouma.


mucherezane wina ndi mnzake, osadandaula:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa