Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 14:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana aamuna ndi aakazi ena.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo Davide anatenga akazi ena ku Yerusalemu, nabala Davide ana aamuna ndi aakazi ena.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Davide adakwatira akazi ena ku Yerusalemu, ndipo adabereka ana enanso aamuna ndi aakazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 14:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anadzitengera akazi aang'ono ena ndi akazi a ulemu ena a ku Yerusalemu, atafikako kuchokera ku Hebroni; ndipo anambadwira Davide ana aamuna ndi aakazi.


Ndipo anali nao akazi mazana asanu ndi awiri, ana aakazi a mafumu, ndi akazi aang'ono mazana atatu; ndipo akazi ake anapambutsa mtima wake.


Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova adamkhazikitsa mfumu ya Israele; pakuti ufumu wake unakwezekadi, chifukwa cha anthu ake Israele.


Maina a ana anali nao mu Yerusalemu ndi awa: Samuwa, ndi Sobabu Natani, ndi Solomoni,


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.


Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.


Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.


Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa