Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 13:13 - Buku Lopatulika

13 M'mwemo Davide sanafike nalo likasa kwao kumzinda wa Davide, koma analipambutsira kunyumba ya Obededomu wa ku Giti.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 M'mwemo Davide sanafike nalo likasa kwao kumudzi wa Davide, koma analipambutsira kunyumba ya Obededomu wa ku Giti.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Motero sadabwere nalo Bokosilo kwao ku mzinda wa Davide, koma adalipatutsira ku nyumba ya Obededomu Mgiti.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 13:13
9 Mawu Ofanana  

ndi Abeeroti anathawira ku Gitaimu; kumeneko amakhalira kufikira lero lino.


Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a mu Israele, anthu zikwi makumi atatu.


Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu?


ndi pamodzi nao abale ao a kulongosola kwachiwiri, Zekariya, Beni, ndi Yaaziele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Uni, Eliyabu, ndi Benaya, ndi Maaseiya, ndi Matitiya, ndi Elifelehu, ndi Mikineya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, odikirawo.


Momwemo Davide, ndi akuluakulu a Israele, ndi atsogoleri a zikwi, anamuka kukwera nalo likasa la chipangano la Yehova, kuchokera kunyumba ya Obededomu mokondwera.


Asafu ndiye mkulu wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeiyele, ndi Semiramoti, ndi Yehiyele, ndi Matitiya, ndi Eliyabu, ndi Benaya, ndi Obededomu, ndi Yeiyele, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;


Ndipo Obededomu anali nao ana, woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinai Sakara, wachisanu Netanele,


Onsewa ndiwo a ana a Obededomu; iwo ndi ana ao, ndi abale ao, anthu odziwa mphamvu yakutumikira, makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri a Obededomu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa