Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 13:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adachita chipasulo ndi Uza; motero anatcha malowo Pereziuza, mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adachita chipasulo ndi Uza; motero anatcha malowo Pereziuza, mpaka lero lino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono Davide adakhumudwa chifukwa chakuti Chauta adaakantha Uza. Ndipo mpaka pano malo amenewo amaŵatchula kuti Pereziuza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 13:11
11 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake ana a Israele samadya mtsempha ya thako ili pa nsukunyu ya ntchafu kufikira lero: chifukwa anakhudza nsukunyu ya ntchafu ya Yakobo pa mtsempha ya thako.


Pomwepo mkwiyo wa Yehova udayaka pa Uza, ndipo Mulungu anamkantha pomwepo, chifukwa cha kusalingiriraku; nafa iye pomwepo pa likasa la Mulungu.


Ndipo Davide anaopa Yehova tsiku lomwelo; nati, Ngati likasa la Yehova lidzafika kwa ine?


Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu.


Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu?


Pakuti, chifukwa cha kusalinyamula inu poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinamfunafuna Iye monga mwa chiweruzo.


Ansembenso, akuyandikiza kwa Yehova adzipatulitse, angawapasule Yehova.


Ndipo Yehova anati, Uyenera kupsa mtima kodi?


Ndipo Mulungu anati kwa Yona, Uyenera kodi kupsa mtima chifukwa cha msatsiwo? Nati iye, Ee, kundiyenera ine kupsa mtima mpaka imfa.


Ndipo Iye anamuika m'chigwa m'dziko la Mowabu popenyana ndi Betepeori; koma palibe munthu wakudziwa kumanda kwake kufikira lero lino.


Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa