Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 13:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo Davide anafunsana ndi akulu a zikwi ndi a mazana, inde atsogoleri ali onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo Davide anafunsana ndi akulu a zikwi ndi a mazana, inde atsogoleri ali onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Davide adapempha nzeru kwa atsogoleri a anthu zikwi, kwa atsogoleri a anthu mazana, ndi kwa mtsogoleri wina aliyense.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 13:1
12 Mawu Ofanana  

Pambuyo pake Davide anamemezanso osankhika onse a mu Israele, anthu zikwi makumi atatu.


Pamenepo mfumu inatumiza anthu, namsonkhanitsira akulu onse a Yuda ndi a mu Yerusalemu.


Awa a ana a Gadi, anali atsogoleri a nkhondo; wamng'ono wa iwo anayang'anira zana limodzi, ndi wamkulu wa iwo anayang'anira chikwi chimodzi.


Pomuka iye ku Zikilagi anapatukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yediyaele, ndi Mikaele, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akulu a zikwi a ku Manase.


Ndi a ana a Isakara, anthu akuzindikira nyengo, akudziwa zoyenera Israele kuzichita, akulu ao ndiwo mazana awiri; ndi abale ao onse anapenyerera pakamwa pao.


Ndiponso akuyandikizana nao mpaka Isakara ndi Zebuloni ndi Nafutali anabwera nao mkate osenzetsa abulu, ndi ngamira, ndi nyuru, ndi ng'ombe, zakudya zaufa, ndi nchinchi zankhuyu, ndi nchinchi zamphesa, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ng'ombe, ndi nkhosa zochuluka; pakuti munali chimwemwe mu Israele.


Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israele, Chikakomera inu, ndipo chikachokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israele, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'mizinda yao yokhala napo podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;


Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo.


Pamenepo mfumu Hezekiya analawira mamawa, nasonkhanitsa akalonga a m'mzinda, nakwera kunka kunyumba ya Yehova.


Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.


Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa