Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:6 - Buku Lopatulika

6 Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Davide anali atanena kuti, “Aliyense amene ayambe kukantha Ayebusi, adzakhala mkulu wolamulira gulu lankhondo.” Tsono Yowabu mwana wa Zeruya ndiye adayamba kupitako, motero adakhala mtsogoleri wankhondo woyamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:6
13 Mawu Ofanana  

Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.


Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.


Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,


Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.


Ndipo nzika za mu Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mzinda wa Davide.


Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mzinda wa Davide.


Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira khamu la nkhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri.


ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.


Adzandifikitsa ndani m'mzinda wa m'linga? Adzanditsogolera ndani ku Edomu?


Nati Aisraele, Kodi mwaona munthu uyu amene anakwera kuno? Zoonadi iye anakwera kuti adzanyoze Israele, ndipo munthu wakumupha iye, mfumu idzamlemeretsa ndi chuma chambiri, nidzampatsa mwana wake wamkazi, nidzayesa nyumba ya atate wake yaufulu mu Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa