Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo nzika za mu Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ayebusiwo adauza Davide kuti, “Kuno sudzaloŵako ai.” Komabe Davideyo adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:5
26 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anakhala m'linga muja, nalitcha mzinda wa Davide. Davide namanga linga pozinga ponse kuyambira ku Milo ndi m'kati momwe.


Momwemo Davide sanafune kudzitengera likasa la Yehova lidze kumzinda wa Davide; koma Davide analipambutsira kunyumba ya Obededomu Mgiti.


Pamenepo anthu anauza mfumu Davide, kuti Yehova wadalitsa banja la Obededomu ndi zake zonse, chifukwa cha likasa la Mulungu. Chomwecho Davide anamuka nakatenga likasa la Mulungu kunyumba ya Obededomu, nakwera nalo kumzinda wa Davide, ali ndi chimwemwe.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsa akulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, akalonga a nyumba za atate a ana a Israele, kwa mfumu Solomoni mu Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova m'mzinda wa Davide, ndiwo Ziyoni.


Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.


Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.


Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mzinda wa Davide.


Pamenepo Solomoni anasonkhanitsira akuluakulu a Israele, ndi akulu onse a mafuko, ndi akalonga a nyumba za makolo a ana a Israele, ku Yerusalemu, kukatenga likasa la chipangano cha Yehova kumzinda wa Davide ndiwo Ziyoni.


Pakuti pamenepo anaika mipando ya chiweruzo, mipando ya nyumba ya Davide.


pakuti Yehova anasankha Ziyoni; analikhumba likhale pokhala pake; ndi kuti,


Koma Ine ndadzoza mfumu yanga Pa Ziyoni, phiri langa loyera.


Phiri la Ziyoni, chikhalidwe chake nchokoma kumbali zake za kumpoto, ndilo chimwemwe cha dziko lonse lapansi, mzinda wa mfumu yaikulu.


koma anasankha fuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda.


Yehova akonda zipata za Ziyoni koposa zokhalamo zonse za Yakobo.


Ndipo adzanena za Ziyoni, uyu ndi uyo anabadwa m'mwemo; ndipo Wam'mwambamwamba ndiye adzaukhazikitsa.


Imbirani zoyamika Yehova, wokhala ku Ziyoni; lalikirani mwa anthu ntchito zake.


monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.


Komatu mwayandikira kuphiri la Ziyoni, ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wa Kumwamba, ndi kwa unyinji wochuluka wa angelo,


Ndipo ndinapenya, taonani, Mwanawankhosayo alikuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi Iye zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai, akukhala nalo dzina lake ndi dzina la Atate wake lolembedwa pamphumi pao.


Koma munthuyo anakana kugonako usiku, nanyamuka, nachoka, nadza pandunji pa Yebusi (ndiwo Yerusalemu); ndi pamodzi naye panali abulu awiri omangirira mbereko; anali nayenso mkazi wake wamng'ono.


Ndipo Davide analankhula ndi anthu akuima pafupi ndi iye, nati, Adzamchitira chiyani munthu wakupha Mfilisti uyu, ndi kuchotsa tonzo lake pakati pa Israele? Pakuti Mfilisti uyu wosadulidwa ndiye yani, kuti azinyoza makamu a Mulungu wamoyo?


Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi chimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa