Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 11:1 - Buku Lopatulika

1 Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Aisraele onse adadzasonkhana kwa Davide ku Hebroni. Adamuuza kuti, “Ifetu ndi inuyo tili magazi amodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 11:1
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Labani anati kwa iye, Eetu, iwe ndiwe fupa langa ndi thupi langa. Ndipo anakhala naye nthawi ya mwezi umodzi.


Koma Abisalomu anatumiza ozonda ku mafuko onse a Israele, kuti, Pakumva kulira kwa lipenga, pomwepo muzinena, Abisalomu ali mfumu ku Hebroni.


Ndipo zitatha izi Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndikwere kunka m'mizinda wina wa Yuda? Ndipo Yehova ananena naye, Kwera. Davide nanena naye, Ndikwere kuti? Ndipo anati, Ku Hebroni.


Ndipo masiku ake akukhala Davide mfumu ya Israele anali zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu ku Hebroni, ndi zaka makumi atatu mphambu zitatu anakhala mfumu ku Yerusalemu.


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


pakuti tili ziwalo za thupi lake.


mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.


Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana aamuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa