1 Mbiri 10:7 - Buku Lopatulika7 Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya mizinda yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya midzi yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Aisraele onse amene anali ku chigwa, ataona kuti gulu lankhondo lathaŵa, ndipo kuti Saulo ndi ana ake aphedwa, nawonso adathaŵa nasiya mizinda yao. Tsono Afilisti aja adabwera nkudzakhala m'menemo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo. Onani mutuwo |