Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Mbiri 10:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anawapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Afilistiwo adapanikiza Saulo ndi ana ake, ndipo adapha Yonatani, Abinadabu ndi Malikisuwa ana a Saulo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 10:2
11 Mawu Ofanana  

Masiku ake Farao Neko mfumu ya Aejipito anakwerera mfumu ya Asiriya ku mtsinje wa Yufurate; ndipo mfumu Yosiya anatuluka kuponyana naye, koma anapha Yosiya ku Megido, atamuona.


Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.


Ndi nkhondoyi inamkulira Saulo, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa chifukwa cha amauta.


Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.


Ndipo Nere anabala Kisi, ndi Kisi anabala Saulo, ndi Saulo anabala Yonatani, ndi Malikisuwa, ndi Abinadabu, ndi Esibaala.


Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;


Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Ndipo Afilisti anapirikitsa, osawaleka Saulo ndi ana ake; ndipo Afilisti anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa