Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 9:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo kunali, zitatha zaka makumi awiri m'mene Solomoni adatsiriza nyumba ziwirizo, ndizo nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ntchito yomanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu idamtengera Solomoni zaka makumi aŵiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu,

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 9:10
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Solomoni anapalana ubwenzi ndi Farao mfumu ya Aejipito, natenga mwana wamkazi wa Farao, nadza naye kumzinda wa Davide, mpaka atamanga nyumba ya iye yekha, ndi nyumba ya Yehova, ndi linga lozinga Yerusalemu.


Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m'chaka chachinai m'mwezi wa Zivi.


Ndipo m'chaka chakhumi ndi chimodzi m'mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.


Koma nyumba ya iye yekha Solomoni anaimanga zaka khumi mphambu zitatu, natsiriza nyumba yake yonse.


Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,


popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu mizinda makumi awiri m'dziko la Galileya.


Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa